AJ creator

AJ creator

Share

content creator

02/05/2026

*MACHIMO ENA AKULU AKULU*

قَالَ عَبْدُ اللَّهِ بْنُ مَسْعُودٍ – رَضِيَ اللَّهُ عَنْهُ –:

أَكْبَرُ الْكَبَائِرِ: الْإِشْرَاكُ بِاللَّهِ، وَالْقُنُوطُ مِنْ رَحْمَةِ اللَّهِ، وَالْيَأْسُ مِنْ رَوْحِ اللَّهِ، وَالْأَمْنُ مِنْ مَكْرِ اللَّهِ. To

_{الطَّبَرِيُّ، التَّفْسِيرُ (الْقُرْآن 4: 31). صَحَّحَهُ ابْنُ كَثِيرٍ فِي تَفْسِيرِهِ لِلْآيَةِ نَفْسِهَا.}_

*Abdullah Bun Mas'ood r, a, adati:*

*Mmachimo akulu akulu;*
1. Shirk
2. Kutaya mtima ndi thandizo la Allah
3. Kutaya mtima ndi chisoni cha Allah
4. Ndikuganiza kuti Plan ya Allah siikuthandiza.

01/05/2026

Ukakupezani uthengawu tiyeni chonde tigawe kumidzi.

01/05/2026

*CHEMWALI ANADANDAULA KUTI ACHIMWENE PA DEEN SAKUMAWALORA KUSALA SUNNAH ZA LOLEMBA NDI LACHINAI" KOMA CHEMWALI ASANAKWATIWE AMASALA MWAKATHITHI NDE ANAFUNSA NGATI BANJALI SIILI NJIRA YOWAKANKHIRA KU JAHANNAM.*

YANKHO
*Ayi chemwali banjali sinjira yokukhanzinzirani ku Jahannam, Hadith ili ya Bukhaar adailandira Abi Hurayrah kuti ndithu mtumiki adalamura motsindika kuti:*
‏ "‏ لاَ يَحِلُّ لِلْمَرْأَةِ أَنْ تَصُومَ وَزَوْجُهَا شَاهِدٌ إِلاَّ بِإِذْنِهِ، وَلاَ تَأْذَنَ فِي بَيْتِهِ إِلاَّ بِإِذْنِهِ، وَمَا أَنْفَقَتْ مِنْ نَفَقَةٍ عَنْ غَيْرِ أَمْرِهِ فَإِنَّهُ يُؤَدَّى إِلَيْهِ شَطْرُهُ ‏"‏‏.‏ وَرَوَاهُ أَبُو الزِّنَادِ أَيْضًا عَنْ مُوسَى عَنْ أَبِيهِ عَنْ أَبِي هُرَيْرَةَ فِي الصَّوْمِ‏.‏
*Zili "Haraam" kwa nkazi kuti asale Sunnah popanda chilolezo cha mwamuna wake pomwe mwamunayo ali pa khomo {sadachoke kupita ku ulendo wokagona konko}, ndipo mzimayi asamulore aliyense kulowa mnyumba ya mwamunayo pokha pokha ndichilolezo cha mwamunayo, ndipo ngati nkazi akupeleka Swadaqah popanda kuuuzidwa ndi mwamuna wake, adzangopeza theka lokha la Sawaab.*
_Sahih al-Bukhari 5195_

@ Chemwali ngati mwamva Hadith-yi' ikumveka bwino kuti mukafuna kusala Sunnah osamuuza mwamuna wanu Swawm yanuyo lamuro lake ndi Haraam, choncho monga ngati ife akuchimuna tikusangalala kuti Ma sha Allah tabaaraka llah. Mukamamva Taqua ndiko kumvera Allah ndi Mtumiki, nde kusala munkasala musana kwatiweko ngatidi inali Taqua tsono tsatirani lamuro limeneli. Kuzimva Taqua powaona ena kufooka kaamba kamaufulu awo mzosayenera kwa okwatirana.

*@* Ena mwa ma Ulamah adati mungathe kusala ngakhale mwamuna ali pa khomo, "koma tsopano akakufunani kaya Lunch, akuyenera kukumasulitsani ndekuti Automatically mumufutura masana lili gaaa. Tsatani Sunnah kuti mukhale safe pa Deen, mwamuna wanu ufulu wake kwa Inu ndiwoopsa koti ngakhale kaya mapemphero ena posakhala kusala' kaya idzakhala Faradh kaya Sunnah ndipo ndizoti Ibaadah imeneyo mungachite nthawi ina, mpatseni Kaye Service mwamunayo. Ndinu nkazi ndipo musaganizire kuti kugonjera kwanu kwa mwamuna wanu ndi loose, zindikirani kt kutero ndi huge Ibaadah.

*@* Tiyelekedzere kuti inali Swalah ya Faradh, nde mwachita Udhu koma mwamuna wakufunani' mpatseni ufulu wake mwamunayo musampangitse kufinyika then mudzasamba mkubwenza Swalah imeneyo ndipo pa izi ma Ulamah ndiwogwirizana. Muyang'anitsitse zomwe mukuyenera kumukanira mwamuna wanu. Ndipo si sangapeze machimo nkazi chifukwa cha kusiya kusala Sunnah.

MALANGIZO ANGA KWA AZICHIMWENE PA DEEN
Udindo umakoma pomwe anthu omwe ukuwalamulirawo ukuwapatsa ufulu. Pomwe anthu omwe ukuwalamulira akumva kukoma ndipomwenso iwe udindo umaumva kutsekemera. Ndikutanthauza kuti azikaziwa tiwapatse ufulu pomwe ife tili adindo awo pasafike pomationa ngati ndife nkhalamo. Mu Qur'an Allah adati:

إِنَّ هَـٰذِهِ تَذْكِرَةٌ ۖ فَمَن شَاءَ اتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِ سَبِيلًا.
*Ndithu Qur'an ndichikumbutso, yemwe akufuna achitenge ndiyo njira yompititsa kwa Mbuye wake.
_Q 76:29_

Ine ndikuona kuti yemwe akufuna kumuopa Allah mpatseni ground likhale lake. Akatopa atiuza.

_Allah akufewetsereni kumvetsa Deen_

01/05/2026

CHEMWALI ANU PA CHIKHULIPILIRO ANAFUNSA NGATI ZILI SUNNAH KUPATSANA MONI WAPA CHANZA IMMEDIATELY AFTER SWALAH YA FARADH

YANKHO
Zopatsana moni pachanza sizinamveke paliponse mmabuku kuti Sunnah, Ife tikuyenera kutsatira Sunnah ndikupewa Bidi'ah mu Deen. Chiwongoko chabwino nde Chiwongoko Cha Muhammad s a w; ndipo zinthu za Satanic nde zomwe zachita kupekedwa pa Deen, Bidi'ah iliyonse ndikusochera ndipo kusochera kulikonse kukamfikitsa Munthu ku Jahannam.

Zomwe amapanga ma Sufiyya kumaumba mkumapatsana chanza ndi ena mwa anthu a Qadriyyah zili baseless.

Allah atipatse kumvetsa Deen

30/04/2026

No squabble or argument is worth it; don't sacrifice your Hereafter for these pettiness. Avoid it and if you can’t, excuse yourself and walk away. Make peace with those you've offended or insulted.

30/04/2026

When you're sad and things are looking bleak, look for a reason to smile. Believe me, you have much to be thankful for. Show gratitude. Thank the Almighty always.

30/04/2026

Hold on to your inner peace no matter how bad things are. That's your greatest strength. Without it, you have nothing. Remember, everything will pass.

29/04/2026

*CHEMWALI PA DEEN AKUFUNA KUDZIWA NGATI PALI DUA YOCHITA AFTER ZINAA, SO THAT UKHULULUKIDWA MKUKHALA NGATI SIUNACHITE ZINAA.* POTENGERA IWO, MU EXPERIENCE YAWO AKUONA KUTI MA SHAYKH AMBIRI SALIOPA TCHIMO LA ZINAA.

*FUNSO*
Kodi pali Dua yomwe akanganya amenewa amadalira? Chonde tiphunzitseni Dua imeneyo.

*YANKHO*
*@* May Allah have mercy! Palibe Dua direct yomwe inakhanzikitsidwa kuti yonena After Zinaa ndikuti munthu akainena adzayeletsedwa ngati sanachite Zinaa, ndipo kulibe zoterozi kumachimo ena posakhala Zinaa whether mu Qur'an or mu Sunnah.

*@* Kuyankhula komati ma Shaykh mngokonda akazi ndikofalikira pakati pa asilamu ndi omwe sali asilamu, izi chifukwa choti Allah analoledza msilamu kukhala ndi nkazi woposa m'modzi pa Qur'an 3:4 ndipo ma Shaykh amachita Practice chilolezo chimenecho kuposa aliyense plus ma shaykh amalimbikitsa kutsatira chilolezochi monga amalimbikitsira Ibaadah Ina.

*@* Zoona zake mzoti palibe mwamuna yemwe amasangalatsidwa ndikukhutitsidwa ndi nkazi m'modzi yekha, ndipo Allah anatsimikizira mu Qur'an kuti awachita amuna kukhala wokonda akazi pa Qur'an 3:14, choncho amuna onse ndiwokonda akazi pachibadwidwe.

*@* Ma shaykh ndi amuna ena omwe amatengera mwai pachilolezochi mmalo mokwatira akazi oposa mmodzi mkumangopanga Zinaa ndikuluza kwawo kwakukulu. Amayenera kugwiritsa mchito chilolezochi kuti afune fune chiyanjo cha Allah. Indee ena mpaka amayankhula kuti mowa wama Shaykh nde zinaaa. Anthu ena ali ndi experience kuti ma shaykh ambiri mngofooka ku tchimo la zinaaa, koti mpaka ena anati kamba koti ma shaykh samamwa mowa, juga, chamba, kuba ndi machimo ena akulu akulu, akuti Zinaa imawaphwekera mwina kaamba koti Zinaa imachitika mdima utakuta Dunia" Wallahul musta'anu nde anasankha Zinaa yoti siimaonekera. *Izi sizili kwama shaykh onse, ndipo 90% yama Shaykh ndiwolungama pomwe 10 or 5% nde omwe samaipeza mitima mpaka akudetsa mbiri zabwino zama shaykh abwino.*

*KODI PALI DUA PAMBUYO PA ZINAA?*
Ayi palibe. Koma Pali njira zotsatidwa kuti munthu akhululukidwe ndikuti asanduke woyera ngati sanachite tchimo la Zinaa or machomo ena ndipo palibe chilango chomwe angalandire akatsatira njirazi.

*IMENEYO NDE TAWBAH*
Machimo anabwelera anthu, ndipo palibe yemwe angatetezeke kumachimo, yemwe wachimwa akumbukire kuthawira kwa Allah mwachangu, kupempha chikhululuko nthawi zonse ndikulapa nthawi zonse.
1. *Musataye mtima poti mwachita Zinaa or tchimo lililonse* pa Qur'an 39:53 Allah akuwaitanira akapolo ake omwe achita Zinaa ndimachimo ena ku chikhululuko Iye mu tanthauzo la Aya akuti: "Tawauze kuti; Oh inu akapolo anga omwe mwazichitira zoipa! {machomo} Musataye mtima zachisoni cha Allah, Ndithu Allah mngokhululuka machimo onse {tchimo lalikulu or laling'ono}; ndipo Iye mngochulukitsa kukhululuka ndiwachisoni.

2. *Kulapa kwanu kukhale koona mtima kusakhale pa lilime pokha, ndipo muzitalikire zomwe zinakugwetserani mu tchimolo. Plus muchilimike pochita Ibaadah, poti ntchito zabwino zimafafaniza machimo.*

3. *Ngati mwalapa kwa Allah m***a mtima si inu wa chiwere werenso. Choncho mulinso ndi mwai wokwatiwa ndi Mwamuna wolungama/nkazi wolungama osati wa Zinaa.*

4. *Munthu wokhulupilira akuyenera kukhala ndi chiyembekedzo chabwino pazabwino zochokera kwa Allah. Ndipo osapempha chitetezo cha Jahannam chokha ayi, koma kupemphanso Jannah chifukwa chakulapa kwake.*

Ladies and Gentlemen! Palinso moyo wokoma pambuyo pa machimo ndipo siinati kukwanira Tawbah ya munthu yemwe walapa koma sanati kusiya tchimolo.

*SHAYKH! INE NDINALAPA KOMA NDACHITANSO TCHIMOLO! ULAPENSO , ULAPENSO , ULAPENSO MPAKA ALLAH AKUPATSE CHITETEZO KUTCHIMOLO, IMENEYO NDE DEEN YANU. SIIMAMUTAYA AMENE WACHIMWA KOMA IMAMUITANA NDIKUMPATSA CHITONTHOZO.*

_Allah atimvere chisoni_

29/04/2026

*ACHIMWENE PA AQEEDAH YOLUNGAMA ANAFUNSA*

*FUNSO*
[4/25, 8:05 AM] +26588...: Achimwene pa Deen muli bwanji?
Kodi ndikuyenera kumupempha nkazi wanga woyamba kuti ndikwatire nkazi wachiwiri?

*YANKHO*
[4/25, 11:05 PM] Amashi...: Ndili bwino, zikomo.

Pa Deen *simukukakamizidwa* kumupempha chilolezo mkazi woyamba kuti mukwatire wachiwiri, kutero kukusonyeza kuti ndiwe chinzake cha Mwamuna' siunakwanire pokhala Mwamuna chifukwa kukwatira nkazi wachiwiri or kuonjezera apo ndi chisankho ndi Decision ya mamuna ndipo siukuyenera kufotokoza zifukwa zokwatilira.

1. *Chilolezo sichofunika mu Sharia*
*@* Qur’an 4:3 imalola kukwatira akazi mpaka 4, malinga ngati mungathe kuchita chilungamo. Palibe ndime imene imati “pempha chilolezo kwa woyamba”. Choncho ngati mutakwatiradi popanda kumuuza, ukwati wachiwiriwo ndi wolondola m’maonekedwe a Sharia.

2. *Koma kumudziwitsa ndi makhalidwe abwino*
Mtumiki ﷺ anati: _“Wabwino mwa inu ndi wabwino kwa akazi ake.”_
*@* Kubisa ukwati kumabweretsa kusakhulupirirana, ndewu, ndi kusweka kwa banja. Akazi ambiri akamva pambuyo pake amapwetekedwa kwambiri. Choncho muuzeni musanakwatire kuti adziwe. Komanso don't challenge her, osachita naye mpikisano pama reaction ake a nsanje, pilirani ndikumvetsa mmene akumvera mu mtima mwake" koma mbali inayo musamalabadire zomwe akudandaulazo.

3. *Chilungamo ndiye chofunikira kwambiri*
Qur’an 4:129: _“Simungathe kuchita chilungamo changwiro pakati pa akazi...”_ koma muyenera kuyesetsa:

- *Nthawi*: Muzigawa masiku mofanana
- *Ndalama*: Muzisamalira onse mofanana malinga ndi kuthekera kwanu
- *Nyumba*: Ngati mmodzi ali ndi nyumba yake, winayonso mpezereni nyumba
- *Chikondi*: Mtima simungawulamulire, koma zochita muzilinganize

*@* Ngati mukudziwa kuti simungathe kuchita chilungamo, Qur’an imati: _“...ngati muopa kuti simudzachita chilungamo, kwatirani mmodzi yekha.”_ 4:3

*Malangizo achimwene:*
1. Pempherani Istikhara kaye
2. Lankhulani ndi mkazi wanu mofatsa. Fotokozareni chidwi chanu, Mverani nkhawa zake.
3. Onetsetsani kuti muli ndi kuthekera kwachuma, kwakuthupi, ndi kwamtima kosamalira mabanja onse awiri

*Chofunika kwambiri*: Ukwati wachiwiri suyenera kuwononga banja loyamba. Ngati kubweretsa chidani ndi chisudzulo, ndiye kuti cholinga cha Sharia sichikwaniritsidwa.

_Ndatha ine m'bale wanu pa Deen, Amashi Iliyas Dines_ ✍️

Want your business to be the top-listed Beauty Salon in Cape Town?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Website

Address

Cape Town