Madyedwe A Machiritso

Madyedwe A Machiritso

Share

Chakudya chanu nthawi zonse chizikhala mankhwala ndipo mankhwala anu odalirika azikhala chakudya!

10/06/2026

CHIMANGA CHOFIIRA
✓Chimanga ichi ichi ndi lokolo weniweni ndipo ndi chabwino zedi.
✓Kufiirako musadabwe ndi chionetsero cha kuchuruka kwa ma "Anthocyanins" komanso "Lutein."
✓"Anthocyanins?" Eya. Awatu ndi ma "Phytochemicals" omwe ndi ofunikira zedi pa nkhani ya kuteteza ndi kulimbana ndi tizirombo toyambitsa khansa! Kodi inu mwatero? Eya ifeyo tikutero!
✓Ma "Anthocyanins" amakuzanso chitetezo cha matenda m'thupi komanso ndi ofunikira zedi m'thupi la munthu yemwe akuvutika ndi nthenda ya shuga.
✓Ndiyetu chimanga ichi ndi chofunika zedi! Inde kaya.
✓Ichotu chimathandizansotu kutsitsa BP, kupereka thanzi labwino la mtima komanso kuletsa ukalamba!
✓Akutitu ndi chophikira thobwa! Nkhani zaketu zikutero. Thobwa lake labwino zedi loti kumwa madzulo basi osadyando nsima iwe ndi kukagona zabwino bwino ndithu.
✓Ndiyetu sitikuimira pamenepo. Chimagachi mukhoza kuphika nsima, chigumu, komanso kusakaniza ndi ufa wa zinthu zina kupangira zakudya zopatsa thanzi!

✓Chaka chino chokha mulime. Mbeu ikupezeka ndi a Eden Green Nursery and Food Forests Ku Ntcheu pa Boma. K5000 per kg.
0991183538.

04/06/2026

Tofu wa soya uyu timadyera nsima kapena mu mpunga

24/05/2026

UBWINO WA TIYI WA CHIDEDE PA NKHANI YOSAMALIRA TSITSI
✓Anthu ambiri amakhumbira tsitsi lidzioneka lakuda bwino, lothinana ndipo lisamayoyoke.
✓Zonsezitu ndi zotheka ndi tiyi wachidede
✓Osati kumwa ayi koma kusambitsa tsitsi lanu ndi tiyi wachidede.
✓Choyenera kuchita ndi kuphika tiyi wa chidede ndipo kenako mudikire azizire pang'ono.
✓Akazizirirapo m***a kusambitsa tsitsi lanu ndi tiyi ameneyu.
✓Chitani izi tsiku ndi tsiku kwa miyezi iwiri kapena itatu.
✓Tiyi ameneyu mukhoza kupanganganso pophatikiza:
1. Matebulo supuni awiri a chidede chonyenyanyenya
2. Tebulo supuni imodzi ya rosemary
3. Tebulo supuni imodzi ya ma cloves.
M***a kuphika izi pogwiritsa ntchito kota litala ya madzi ndi kuphika.
✓Kenako phulani ndi kusefa.
✓Gwiritsani ntchito 50mls potsukira tsitsi lanu pochita chomakhula ndi mmanja (massage).
✓Otsalayo sungani mu fridge ndipo mudzagwiritsa ntchito mawa lake ndi masiku otsatira.
✓Ngati mulibe rosemary ndi ma cloves; gwiritsani ntchito chidede chokha basi!
✓Akazi inu njira yosatha ndalama iyi, yosavuta, yachilengedwe yosamalira tsitsi lanu.

Zikomo.

EDEN GREEN NURSERY AND FOOD FOREST
0991183538
NTCHEU.

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 21/05/2026

NGATI SIMUKUDZIWA
✓Chimanga ichi ndi lokolo weniweni kusiyana ndi china chonse chija timati lokolo chija.
✓Chimanga ichichi chiri ndi ubwino waukuru zedi pa thanzi labwino kusiyana ndi chachikasu chija.
✓Chimanga ichichi ndi bwenzi leni leni la ubongo kusiyana ndi chachikasu chija.
✓Ngati mukufuna thanzi labwino nsima yopatsa thanzi ndi yachimanga chimenechi.

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 20/05/2026

UBWINO WA CHIDEDE PA THANZI LABWINO LA CHIWINDI
✓Chidede chiri ndi kuthekera kwakukuru kopereka thanzi labwino kuchiwindi.
✓Choncho kumwa tiyi kapena juice wa chidede ndi kothandiza ndithu kuti chiwindi chidzigwira bwino ntchito yake yochotsa poizoni mmagazi.
✓Kumwa tambula imodzi ya tiyi wachidede patsiku ndi kothandiza.
✓Viikani chidede pang'ono chabe mu tambula imodzi ya madzi otentha.
✓Dikirani kwa 20 minutes ndipo kenako sefani ndi kumwa.

Usiku wabwino

EDEN GREEN NURSERY AND FOOD FOREST
0991183538
NTCHEU

17/05/2026

CHIDEDE
✓Ino ndi nthawi yokolola chidede
✓Eden Green Nursery ikukulimbikitsani kuti mulime chidede
✓Chidede ndi chofunikira zedi
✓Osazengereza ayi.
✓Icho chimasungunura magazi ndikupangitsa kuti adziyenda bwino m'mitsempha.

EDEN GREEN NURSERY AND FOOD FOREST
0991183538
NTCHEU

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 14/05/2026

GALAGADEYA WA PAPAYA
(Pawpaw Dilla)
✓Kunja kuno kulitu galagadeya wamkuru zedi ngati papaya.
✓Ndiye zipatso zake zimakoma, zofewa; ndipo ndizoyenera anthu amene ali ndi mavuto a mmimba komanso anthu amene adwalika zedi koma afunika atadya.
✓Mtengo wake umayanga kwambiri ndipo ndi ofunikira support yabwino zedi.

✓Iwo amene angafune mbeu yake ayimbire ku Eden Green Nursery ya ku Ntcheu.
✓Mbeu imeneyi ikupezeka pa mtengo wa k2500
✓Imbani pa 0991183538

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 14/05/2026

ROSEMARY TIYI
✓Lero tikambirane za momwe tiyi wa rosemary amathandizira pa kagwiridwe ntchito ka ubongo.
✓Kumbukirani kuti ndinafotokoza kuti rosemary ndi mankhwala abwino zedi a nthenda ya kuyiwala.
✓Kodi izi zimatheka bwanji?
✓Risemary ali ndi ma chemicals amene amathandiza kuteteza ubongo komanso kopangitsa ubongo kuti udzigwira bwino ntchito, makamaka kukumbukira zinthu.
✓Chinthu china chomwe rosemary amachita ku mbali ya ubongo ndi kuthandiza kuti magazi adziyenda bwino mu ubongo! Izi zimafunikira zedi kuti ubongo udzilandira mpweya (Oxygen) ochuruka. Ngati ubongo ukulandira oxygen ochuruka umakhala ndi mphamvu yaikuru yokumbukira zinthu komanso umaeonjenzera chidwi cha munthu pa maphunziro.
✓Anthu amene ali ndi nthenda yoyiwala zinthu akuyenera kumwa makapu awiri patsiku a tiyi wa rosemary kwa masiku 30.
✓Ngati munthu akungodzifunira thanzi labwino la ubongo ndibwino kumwa tiyi wa rosemary makapu awiri kapena atatu pa mlungu. Osamwa mowirikiza!
✓Popanga tiyi wa rosemary chitani izi:
1. Wiritsani kapu imodzi ya madzi abwino.
2. Viikani tiyi supuni imodzi kapena awiri a masamba a rosemary owuma kapena awisi m'kapu yamadziyo
3. Bvindikirani ndipo mudikire kwa 20 minutes.
4. Kenako sefani ndipo mukhoza kumwa.
✓M***a kumwa mmawa ndi madzulo.
✓Musatsire shuga koma mukhoza kukometsera ndi uchi kapena Stevia.
✓Akazi oyembekenzera asamwe tiyi wa rosemary.
✓Anthu amene akumwa mankhwala a kuchipatala otsitsa BP komanso a shuga asamwe tiyi wa rosemary popanda kufunsa uphungu kwa dotolo wawo.

Zikomo!

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 13/05/2026

MPHODZA
✓Ngati kulinso nyemba zabwino pansi pano ndizo MPHODZA. Ndikhulupirira kuti anthu a kwa Ndungunya cha ku miseu folo ku Phalombe uko andimvereza.
✓Koma chokhumudwitsa ndi MPHODZA ndiko kuvuta kupsya. Kulimba monga mchenga.
✓Njira yabwino yodyera mphodza ndiyo kupanga chipere. Chipere chake chabwino zedi.
✓Koma ine ndekha, kuno ku Ntcheu, ndimapanga chimera cha mphodza.
✓Chimera cha mphodza ndi ndiwo zabwino zedi. MPHODZA zomeretsa zimakhala ndi ma vitamins ochuruka ndipo zimathandiza pa mavuto osiyana siyana m'thupi!
✓Ndikhulupirira anthu a ku Phalombe andimvetsa; ndipo ayamba kudya mphodza zomeretsa!

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 13/05/2026

ROSEMARY
✓Rosemarry ndi chimodzi mwa zomera zofunikira zedi.
✓Lerotu anthu ambiri tikudwala nthenda yoyiwala zinthu.
✓Ambiri panopa akuiwala ngakhale cholinga cheni cheni chokhalira ndi moyo.
✓Choopsa zedi ndicho chakuti anthu sadziwa kuti kuli nthenda imeneyi ndipo kuti nthendayi ndi yokhudzana ndi ubongo.
✓Komabe ngakhale ziri choncho; Kunja kuno kuli Rosemary!
✓Ndi spice komanso herbal
✓Kunukhiritsa mpunga ndicho chomwe ambiri amamudziwira Rosemary. Anzungu ndi amwenye anapalana naye ubwezi Rosemary.
✓Tikhala tikukambirana zambiri zokhudzana ndi Rosemary.
✓Koma chinthu chimodzi nachi; Rosemary ndi mankhwala eni eni a nthenda ya kuyiwala!

Want your business to be the top-listed Beauty Salon in Ntcheu?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Telephone

Website

Address


Ntcheu